Mtsogoleri wa bungwe la Super League of Malawi (SULOM) Brigadier General Gilbert Mittawa wapempha matimu omwe amasewera mu ligi yayikulu kuti apeze ma bwalo a zamasewero odalirika.
Malinga ndi Brigadier General Gilbert Mittawa kukhala ndi malo abwino otetezeka opangirapo ma pulakatesi ndi njira imodzi yopititsa masewero a mpira wamiyendo patsogolo.Iye walakhula izi lolemba pa masewero omalinza a mpikisano wa Central Region Elite Teams Easter Bonanza a Goshen City Dedza Dynamos FC ndi Civil Service United pa bwalo la zamasewero la Dedza.

Brigadier General Gilbert Mittawa wati ndizokhumudwitsa kuti ma bwalo ambiri akumagwiritsidwa ntchito kwambiri,zomwe zikuyika chiopsenzo pakakozekeledwe ka matimu.Iye wati pakuyenera kupereka chilolenzo kwa ma timu omwe amagwiritsa ntchito ma bwalo kuti adziwonetsetsa akukhala patsogolo osamala ma bwalo wa.