Skip to Content

Kazembe wa dziko la Japan ku Malawi ayendera sukulu ya Chikangulu Community Day Sekondale ku Chiradzulo

April 9, 2026 by
Phalombe FM

 Kazembe wa dziko la Japan ku Malawi,Yasushi Naito,lachiwiri adayendera sukulu   ya Chikangulu Community Day Sekondale  ku Chiradzulo.Mwazina cholinga cha ulendo wu chinali kufuna kukayamikira ntchito ya mahunziro momwe ikuyendera pa sukulu yi.Sukulu yi yomwe idamangidwa kudzera ku ndondomeko ya Grant Assitance for Grassroots Human Security Project ya m’dziko la Japan, idaperekedwa ku dziko lino chaka cha 2018.

Polakhula ku gulu la anthu lomwe lidasokhana pa sukulu ya Chikangula CDSS, Naito wati ndiokondwa kuwona kuti sukulu yi ikusamalidwa bwino komaso maphunziro akuyenda bwino.

yu adayamikiranso ntchito za chitukuko zomwe phungu wa delali a Joseph Mwanamveka omwe ndi nduna ya za chuma.Malinga ndi Naito a kupatula kupereka mipando pa sukulu yi, nduna yi idagwira ntchito yayikulu yothandizira kumangidwa kwa sukulu yi.Mwanamveka wayamikira dziko la Japan pomanga sukulu yi, ponena kuti kupenzeka kwa sukulu yi kuthandinzira kwambiri kupititsa patsogolo ntchito za maphunziro pakati pa anthu ake.

in News
Share this post
Archive